Ekisodo 8:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Pa tsiku limenelo ndidzapatula dera la Goseni kumene kuli anthu anga, kuti kusakhale tizilombo toyamwa magazi.+ Ndidzatero kuti udziwe kuti ine ndine Yehova, ndipo ndili ndi mphamvu padziko lonse lapansi.+ Ekisodo 10:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Anthu sanathe kuonana ndipo palibe anachoka pakhomo pake kwa masiku atatu. Koma kumene ana onse a Isiraeli anali kukhala kunali kuwala.+ Ekisodo 11:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Koma galu sadzauwa aliyense wa ana a Isiraeli, sadzauwa munthu kapena chiweto,+ kuti mudziwe kuti Yehova akhoza kuchitira ana a Isiraeli zinthu zosiyana ndi zimene angachitire Aiguputo.’+ Ekisodo 12:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Magaziwo adzakhala chizindikiro panyumba zimene mudzakhalamo. Ndipo ine ndidzaona magaziwo ndi kukupitirirani,+ choncho mliri sudzakugwerani ndi kukuwonongani pamene ndikukantha dziko la Iguputo. Yesaya 65:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Atumiki anga adzadya,+ koma inuyo mudzakhala ndi njala.+ Atumiki anga adzamwa,+ koma inuyo mudzakhala ndi ludzu.+ Atumiki anga adzasangalala,+ koma inuyo mudzachita manyazi.+ Malaki 3:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Ndithu, anthu inu mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa+ ndiponso pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sanatumikirepo Mulungu.”+
22 Pa tsiku limenelo ndidzapatula dera la Goseni kumene kuli anthu anga, kuti kusakhale tizilombo toyamwa magazi.+ Ndidzatero kuti udziwe kuti ine ndine Yehova, ndipo ndili ndi mphamvu padziko lonse lapansi.+
23 Anthu sanathe kuonana ndipo palibe anachoka pakhomo pake kwa masiku atatu. Koma kumene ana onse a Isiraeli anali kukhala kunali kuwala.+
7 Koma galu sadzauwa aliyense wa ana a Isiraeli, sadzauwa munthu kapena chiweto,+ kuti mudziwe kuti Yehova akhoza kuchitira ana a Isiraeli zinthu zosiyana ndi zimene angachitire Aiguputo.’+
13 Magaziwo adzakhala chizindikiro panyumba zimene mudzakhalamo. Ndipo ine ndidzaona magaziwo ndi kukupitirirani,+ choncho mliri sudzakugwerani ndi kukuwonongani pamene ndikukantha dziko la Iguputo.
13 Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Atumiki anga adzadya,+ koma inuyo mudzakhala ndi njala.+ Atumiki anga adzamwa,+ koma inuyo mudzakhala ndi ludzu.+ Atumiki anga adzasangalala,+ koma inuyo mudzachita manyazi.+
18 Ndithu, anthu inu mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa+ ndiponso pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sanatumikirepo Mulungu.”+