Deuteronomo 28:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 “Yehova adzachititsa adani ako amene adzakuukira kugonja pamaso pako.+ Pobwera kwa iwe adzadutsa njira imodzi, koma pothawa pamaso pako, adzadutsa njira 7.+ Deuteronomo 32:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Kodi munthu mmodzi angathamangitse bwanji anthu 1,000,Kapena anthu awiri angapitikitse bwanji anthu 10,000?+ N’zosatheka, pokhapokha Thanthwe lawo litawagulitsa,+Komanso ngati Yehova atawapereka. Yoswa 23:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Munthu mmodzi yekha wa inu adzathamangitsa anthu 1,000,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndiye akukumenyerani nkhondo,+ monga mmene anakulonjezerani.+ Oweruza 7:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Ndiyeno amuna 300 aja anawagawa m’magulu atatu. Aliyense anamupatsa lipenga la nyanga ya nkhosa+ ndi mtsuko waukulu wopanda kanthu, ndipo m’mitsukomo anaikamo miyuni. Oweruza 15:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Zitatero, anapeza fupa laliwisi la nsagwada za bulu wamphongo, n’kukantha nalo amuna 1,000.+ 1 Mbiri 11:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Abisai+ m’bale wake wa Yowabu+ anali mtsogoleri wa amuna atatu. Iye ananyamula mkondo n’kupha anthu 300 ulendo umodzi, ndipo anali wotchuka ngati amuna atatu aja.
7 “Yehova adzachititsa adani ako amene adzakuukira kugonja pamaso pako.+ Pobwera kwa iwe adzadutsa njira imodzi, koma pothawa pamaso pako, adzadutsa njira 7.+
30 Kodi munthu mmodzi angathamangitse bwanji anthu 1,000,Kapena anthu awiri angapitikitse bwanji anthu 10,000?+ N’zosatheka, pokhapokha Thanthwe lawo litawagulitsa,+Komanso ngati Yehova atawapereka.
10 Munthu mmodzi yekha wa inu adzathamangitsa anthu 1,000,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndiye akukumenyerani nkhondo,+ monga mmene anakulonjezerani.+
16 Ndiyeno amuna 300 aja anawagawa m’magulu atatu. Aliyense anamupatsa lipenga la nyanga ya nkhosa+ ndi mtsuko waukulu wopanda kanthu, ndipo m’mitsukomo anaikamo miyuni.
20 Abisai+ m’bale wake wa Yowabu+ anali mtsogoleri wa amuna atatu. Iye ananyamula mkondo n’kupha anthu 300 ulendo umodzi, ndipo anali wotchuka ngati amuna atatu aja.