Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 1:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Iye aziika dzanja lake pamutu pa nsembe yopserezayo ndipo idzalandiridwa+ kuti iphimbe machimo ake.+

  • Levitiko 4:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Mafuta onse a mbuziyo aziwatentha paguwa lansembe mofanana ndi mafuta a nsembe yachiyanjano.+ Pamenepo wansembe aziphimba tchimo la mtsogoleriyo,+ ndipo azikhululukidwa.

  • Levitiko 4:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Kenako azichotsa mafuta onse+ a mbuziyo, monga mmene amachotsera mafuta a nsembe yachiyanjano.+ Pamenepo wansembe azitentha mafutawo paguwa lansembe kuti likhale fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+ Ndiyeno wansembe aziphimba tchimo la munthuyo, ndipo azikhululukidwa.+

  • Levitiko 6:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Ndiyeno wansembe aziphimba machimo+ a munthuyo pamaso pa Yehova, ndipo azikhululukidwa chilichonse mwa zonse zimene angachite zom’palamulitsa.”

  • Levitiko 16:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Pakuti pa tsiku limeneli machimo anu adzaphimbidwa+ kuti muyesedwe oyera. Mudzakhala oyeretsedwa ku machimo anu onse pamaso pa Yehova.+

  • Numeri 15:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Wansembe apereke nsembe yophimba tchimo la munthuyo, amene walakwira Yehova mosazindikira, kuti akhululukidwe.+

  • Akolose 1:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Mwa Mwana wakeyo, tinamasulidwa ndi dipo,* kutanthauza kuti machimo athu anakhululukidwa.+

  • 1 Yohane 2:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Iye ndi nsembe+ yophimba+ machimo athu.+ Osati athu+ okha, komanso a dziko lonse lapansi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena