Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 22:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Tsopano tabwerani chonde, mudzanditembererere+ anthuwa chifukwa ndi amphamvu kuposa ineyo, kuti mwina ndingawagonjetse n’kuwapitikitsa m’dziko lino. Ndikudziwa kuti munthu amene inu mwamudalitsa, amakhaladi wodalitsika, ndipo munthu amene mwamutemberera, amakhaladi wotembereredwa.”+

  • Numeri 23:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Pamenepo Balamu anayamba kulankhula mwa ndakatulo,+ kuti:

      “Balaki mfumu ya Mowabu yandiitana kuchokera ku Aramu,+

      Kuchokera kumapiri a kum’mawa, kuti:

      ‘Bwera, udzanditembererere Yakobo.

      Bwera, udzaitanire tsoka pa Isiraeli.’+

  • Numeri 23:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Balaki atamva zimenezi anafunsa Balamu kuti: “N’chiyani mwandichitachi? Ndinakutengani kuti mudzatemberere adani anga, koma inu mwawadalitsa kwambiri.”+

  • Numeri 24:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pamenepo Balaki anapsera mtima Balamu n’kuwomba m’manja.+ Kenako anauza Balamu kuti: “Ndinakuitana kuti udzatemberere+ adani anga, koma iwe wawadalitsa kwambiri katatu konseka!

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena