4 Chifukwa chake n’chakuti, sanakuthandizeni+ ndi mkate ndi madzi pamene munali pa ulendo mutatuluka mu Iguputo,+ ndiponso chifukwa chakuti analemba ganyu Balamu mwana wa Beori, amene kwawo ndi ku Petori ku Mesopotamiya kuti akutemberereni.+
9 Kenako Balaki mwana wa Zipori,+ mfumu ya Mowabu, ananyamuka kukamenyana ndi Isiraeli.+ Iye anaitanitsa Balamu, mwana wa Beori, ndi kumuuza kuti akutemberereni.+