Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 7:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikika pamaso pako mpaka kalekale. Mpando wako wachifumu udzakhazikika mpaka kalekale.”’”+

  • Yesaya 9:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Ulamuliro wake wangati wa kalonga udzafika kutali+ ndipo mtendere sudzatha+ pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wake, kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndi kukhala wolimba pogwiritsa ntchito chilungamo,+ ndiponso pogwiritsa ntchito mtima wowongoka,+ kuyambira panopa mpaka kalekale.* Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+

  • Yesaya 14:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Iweyo wanena mumtima mwako kuti, ‘Ndikwera kumwamba.+ Ndikweza mpando wanga wachifumu+ pamwamba pa nyenyezi+ za Mulungu. Ndikhala paphiri lokumanapo+ kumapeto kwenikweni kwa madera a kumpoto.+

  • Yeremiya 23:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “ndipo Davide ndidzamuutsira mphukira yolungama.+ Ndithudi mfumu idzalamulira+ m’dzikoli ndi kuchita zinthu mozindikira, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+

  • Ezekieli 21:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Ine ndidzawononga, ndidzawononga, ndidzawononga ufumu.*+ Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa wina aliyense kufikira atabwera amene ali woyenerera mwalamulo kuutenga,+ ndipo ndidzaupereka kwa iye.’+

  • 2 Petulo 1:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Choncho mawu aulosiwa+ ndi odalirika kwambiri,+ ndipo mukuchita bwino kuwaganizira mozama. Mawu amenewo ali ngati nyale+ imene ikuwala mu mdima, m’mitima yanu, mpaka m’bandakucha, nthanda*+ ikadzatuluka.

  • Chivumbulutso 22:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 “‘Ine Yesu, ndinatumiza mngelo wanga kudzachitira umboni zinthu izi kwa inu, kuti zithandize mipingo. Ine ndine muzu+ ndi mbadwa+ ya Davide. Ndinenso nthanda yonyezimira.’”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena