5 kapena akapita ndi mnzake kuthengo kukafuna nkhuni, ndipo wakweza dzanja lake kuti adule mtengo ndi nkhwangwa koma nkhwangwayo yaguluka mumpini wake+ n’kukantha mnzake ndi kumupha, wopha mnzakeyo azithawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi kuti akhale ndi moyo.+