53 Alevi azimanga mahema awo mozungulira chihema cha Umboni kuti mkwiyo+ wa Mulungu usawayakire ana a Isiraeli. Aleviwo azitumikira pachihema cha Umbonicho.”+
16 Koma atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza+ mpaka kufika pom’pweteketsa.+ Choncho anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita m’kachisi wa Yehova kukafukiza paguwa lansembe zofukiza.+