Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 18:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Koma mwa anthu onsewa, usankhe amuna oyenerera,+ oopa Mulungu,+ okhulupirika,+ odana ndi kupeza phindu mwachinyengo.+ Amenewa uwaike kukhala otsogolera anthuwa, ndipo pakhale atsogoleri a magulu a anthu 1,000,+ atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10.+

  • Numeri 1:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Amenewa ndiwo osankhidwa a khamu la anthuwo, atsogoleri a mafuko+ a makolo awo. Aliyense wa iwo ndi mtsogoleri wa anthu masauzande mu Isiraeli.”+

  • Numeri 7:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Pamenepo atsogoleri a Isiraeli,+ amene anali atsogoleri a nyumba za makolo awo, anapereka zopereka zawo.+ Anatero monga atsogoleri a mafuko awo, monganso oyang’anira anthu amene anawerengedwa aja.

  • Deuteronomo 1:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Choncho ndinatenga atsogoleri a mafuko anu, amuna anzeru ndi ozindikira n’kuwaika kukhala atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50, atsogoleri a magulu a anthu 10, ndi akapitawo a m’mafuko anu.+

  • Deuteronomo 5:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 “Ndiyeno mutangomva mawu amenewo kuchokera pamalo amdima, phiri likuyaka moto,+ munabwera kwa ine. Atsogoleri onse a mafuko anu ndi akulu anu onse anabwera kwa ine.

  • Deuteronomo 31:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Pamenepo Mose analemba chilamulo chimenechi+ ndi kuchipereka kwa ansembe, ana a Levi,+ onyamula likasa la pangano la Yehova.+ Anachiperekanso kwa akulu onse a Isiraeli.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena