27 Atafika kumeneko anayamba kuliza lipenga la nyanga+ ya nkhosa m’dera lamapiri la Efuraimu.+ Iye ali patsogolo, ana a Isiraeli anatsika naye limodzi kuchoka m’dera lamapirilo.
12 Taonani, ife patsogolo pathu pali Mulungu woona+ ndi ansembe ake,+ ndi malipenga+ otiitanira ku nkhondo yomenyana nanu. Inu ana a Isiraeli, musamenyane ndi Yehova Mulungu wa makolo anu,+ chifukwa simupambana.”+