Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 21:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Ndipo inuyo mudzachotsa mlandu wa magazi a munthu wosalakwa pakati panu,+ chifukwa mudzakhala mutachita choyenera pamaso pa Yehova.+

  • 2 Mafumu 21:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Manase anakhetsanso magazi osalakwa ochuluka zedi,+ mpaka magaziwo anadzaza nawo Yerusalemu kuyambira koyambirira mpaka kumapeto, kuwonjezera pa tchimo lake limene anachimwitsa nalo Yuda mwa kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+

  • Miyambo 6:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Maso odzikweza,+ lilime lonama,+ manja okhetsa magazi a anthu osalakwa,+

  • Yeremiya 7:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 ngati simudzapondereza mlendo wokhala pakati panu, mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye,+ komanso ngati simudzakhetsa magazi a munthu wopanda mlandu m’dziko lino,+ ndiponso ngati simudzatsatira milungu ina, zimene zingakubweretsereni tsoka,+

  • Yona 1:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Pamenepo anthuwo anafuulira Yehova ndi kunena kuti:+ “Chonde inu Yehova, musalole kuti tiwonongeke chifukwa cha munthu uyu! Musaike pa ife mlandu wa magazi a munthu wosalakwa,+ chifukwa zonsezi zachitika pokwaniritsa chifuniro chanu, inu Yehova!”+

  • Mateyu 27:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Iye anati: “Ndachimwa popereka munthu wolungama.”*+ Koma iwo anamuyankha kuti: “Ife sizikutikhudza zimenezo. Udziwa wekha chochita!”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena