Yeremiya 9:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Choncho Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndidzadyetsa anthu amenewa chitsamba chowawa,+ ndipo ndidzawamwetsa madzi apoizoni.+ Hoseya 10:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 “Iwo amalankhula mawu opanda pake, amachita malumbiro abodza,+ amachita mapangano+ ndipo kusalungama kwafalikira ngati zomera zakupha m’mizere ya m’munda.+ Amosi 6:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 “‘Kodi mahatchi angathamange pathanthwe, kapena kodi munthu angalime pathanthwe ndi ng’ombe? Anthu inu mwakana chilungamo,+ choncho mwachititsa moyo wa anthu kukhala wowawa. Machitidwe 8:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Pakuti ndaona kuti ndiwe ndulu yaululu+ ndipo mwa iwe mwadzaza kusalungama.”+ Aheberi 12:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Pochita zimenezo, muonetsetse kuti wina asalandidwe kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu,+ komanso kuti pakati panu pasatuluke muzu wapoizoni+ woyambitsa mavuto, ndi kuti ambiri asaipitsidwe nawo.+
15 Choncho Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndidzadyetsa anthu amenewa chitsamba chowawa,+ ndipo ndidzawamwetsa madzi apoizoni.+
4 “Iwo amalankhula mawu opanda pake, amachita malumbiro abodza,+ amachita mapangano+ ndipo kusalungama kwafalikira ngati zomera zakupha m’mizere ya m’munda.+
12 “‘Kodi mahatchi angathamange pathanthwe, kapena kodi munthu angalime pathanthwe ndi ng’ombe? Anthu inu mwakana chilungamo,+ choncho mwachititsa moyo wa anthu kukhala wowawa.
15 Pochita zimenezo, muonetsetse kuti wina asalandidwe kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu,+ komanso kuti pakati panu pasatuluke muzu wapoizoni+ woyambitsa mavuto, ndi kuti ambiri asaipitsidwe nawo.+