Levitiko 26:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Ndidzatumiza zilombo zakutchire pakati panu,+ ndipo zidzakupherani ana anu+ ndi ziweto zanu, ndi kuchepetsa chiwerengero chanu, moti m’misewu yanu mudzakhala mopanda anthu.+ Yeremiya 15:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 “‘Ndidzawagwetsera masoka a mitundu inayi,’+ watero Yehova. ‘Ndidzawatumizira lupanga kuti liwaphe, agalu kuti akoke mitembo yawo, zolengedwa zouluka zam’mlengalenga+ ndi zilombo zakutchire kuti ziwadye ndi kuwawononga. Ezekieli 5:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Ndidzakutumizirani njala ndi zilombo zakupha+ ndipo zidzakupherani ana anu. Mliri+ ndi magazi+ zidzadutsa pakati panu ndipo ine ndidzakubweretserani lupanga.+ Ineyo Yehova ndi amene ndanena zimenezi.’”
22 Ndidzatumiza zilombo zakutchire pakati panu,+ ndipo zidzakupherani ana anu+ ndi ziweto zanu, ndi kuchepetsa chiwerengero chanu, moti m’misewu yanu mudzakhala mopanda anthu.+
3 “‘Ndidzawagwetsera masoka a mitundu inayi,’+ watero Yehova. ‘Ndidzawatumizira lupanga kuti liwaphe, agalu kuti akoke mitembo yawo, zolengedwa zouluka zam’mlengalenga+ ndi zilombo zakutchire kuti ziwadye ndi kuwawononga.
17 Ndidzakutumizirani njala ndi zilombo zakupha+ ndipo zidzakupherani ana anu. Mliri+ ndi magazi+ zidzadutsa pakati panu ndipo ine ndidzakubweretserani lupanga.+ Ineyo Yehova ndi amene ndanena zimenezi.’”