Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 26:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Ndidzatumiza zilombo zakutchire pakati panu,+ ndipo zidzakupherani ana anu+ ndi ziweto zanu, ndi kuchepetsa chiwerengero chanu, moti m’misewu yanu mudzakhala mopanda anthu.+

  • Deuteronomo 32:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Adzalefuka ndi njala+ ndi kuwonongeka ndi matenda otentha thupi koopsa,+

      Ndi chiwonongeko chowawa.+

      Ndidzawatumizira zilombo za mano ataliatali,+

      Pamodzi ndi njoka zapoizoni za m’fumbi.+

  • 2 Mafumu 17:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Atayamba kukhala mmenemo, iwo sanaope+ Yehova. Choncho Yehova anatumiza mikango+ pakati pawo ndipo inapha ena a iwo.

  • Ezekieli 14:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Zidzateronso ndikadzabweretsa ziweruzo zanga zinayi izi zowononga:+ lupanga, njala, zilombo zolusa zakutchire ndi mliri.+ Ndidzatumiza zimenezi mu Yerusalemu kuti zikaphemo anthu ndi ziweto.+

  • Ezekieli 33:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 “Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo, ndithu anthu amene ali m’malo owonongedwa adzaphedwa ndi lupanga.+ Munthu amene ali kutchire ndidzam’pereka kwa chilombo cholusa kuti akhale chakudya chake.+ Anthu amene ali m’malo otetezeka ndi m’mapanga+ adzafa ndi mliri.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena