Ekisodo 23:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Iwe usanafike, ndidzachititsa anthuwo mantha*+ ndipo Ahivi, Akanani ndi Ahiti adzathawiratu pamaso pako.+ Deuteronomo 7:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 “Yehova Mulungu wako akadzakulowetsa m’dziko limene ukupita kukalitenga kukhala lako,+ adzakuchotsera mitundu ikuluikulu.+ Adzakuchotsera Ahiti,+ Agirigasi,+ Aamori,+ Akanani,+ Aperezi,+ Ahivi+ ndi Ayebusi,+ mitundu 7 ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa iwe.+ Deuteronomo 9:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 “Tamverani Aisiraeli inu, lero mukuwoloka Yorodano+ kulowa m’dziko limene mukukalilanda kwa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa inuyo.+ Mukukalanda mizinda ikuluikulu yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri yofika kumwamba.+ Yoswa 3:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Atafika, Yoswa anati: “Mukaona zimene zichitike pano, mudziwa kuti Mulungu wamoyo alidi pakati panu.+ Mudziwanso kuti iye adzathamangitsadi pamaso panu Akanani, Ahiti, Ahivi, Aperezi, Agirigasi, Aamori ndi Ayebusi.+ Salimo 44:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Munapitikitsa anthu a mitundu ina ndi dzanja lanu,+Ndipo m’malo mwawo munakhazikitsa anthu anu.+Munagonjetsa mitundu ya anthu ndi kuipitikitsa.+
28 Iwe usanafike, ndidzachititsa anthuwo mantha*+ ndipo Ahivi, Akanani ndi Ahiti adzathawiratu pamaso pako.+
7 “Yehova Mulungu wako akadzakulowetsa m’dziko limene ukupita kukalitenga kukhala lako,+ adzakuchotsera mitundu ikuluikulu.+ Adzakuchotsera Ahiti,+ Agirigasi,+ Aamori,+ Akanani,+ Aperezi,+ Ahivi+ ndi Ayebusi,+ mitundu 7 ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa iwe.+
9 “Tamverani Aisiraeli inu, lero mukuwoloka Yorodano+ kulowa m’dziko limene mukukalilanda kwa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa inuyo.+ Mukukalanda mizinda ikuluikulu yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri yofika kumwamba.+
10 Atafika, Yoswa anati: “Mukaona zimene zichitike pano, mudziwa kuti Mulungu wamoyo alidi pakati panu.+ Mudziwanso kuti iye adzathamangitsadi pamaso panu Akanani, Ahiti, Ahivi, Aperezi, Agirigasi, Aamori ndi Ayebusi.+
2 Munapitikitsa anthu a mitundu ina ndi dzanja lanu,+Ndipo m’malo mwawo munakhazikitsa anthu anu.+Munagonjetsa mitundu ya anthu ndi kuipitikitsa.+