Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 23:40
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 40 Pa tsiku loyambali muzitenga zipatso zabwino kwambiri, masamba a kanjedza,+ nthambi zikuluzikulu za masamba ambiri ndi mitengo ya msondodzi ya m’chigwa.* Mukatero muzisangalala+ kwa masiku 7 pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

  • Deuteronomo 12:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ndipo muzisangalala pamaso pa Yehova Mulungu wanu,+ inuyo ndi ana anu aamuna, ana anu aakazi, akapolo anu aamuna, akapolo anu aakazi ndi Mlevi wokhala mumzinda wanu, chifukwa iye alibe gawo kapena cholowa monga inu.+

  • Deuteronomo 26:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Uzikasangalala+ chifukwa cha zabwino zonse zimene Yehova Mulungu wako wapatsa iwe ndi nyumba yako, zimene wapatsa iweyo komanso Mlevi ndi mlendo wokhala pakati panu.+

  • Nehemiya 8:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Nehemiya anapitiriza kunena kuti: “Pitani mukadye zinthu zonona, kumwa zinthu zokoma ndi kugawa chakudya+ kwa anthu amene sanathe kudzikonzera chakudya, pakuti lero ndi tsiku lopatulika kwa Ambuye wathu. Choncho musadzimvere chisoni pakuti chimwemwe chimene Yehova amapereka ndicho malo anu achitetezo.”

  • Nehemiya 8:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Choncho mpingo wonse wa anthu amene anabwerera kuchokera ku ukapolo anamanga misasa ndi kukhala m’misasayo. Panali chisangalalo chachikulu kwambiri+ chifukwa chakuti ana a Isiraeli anali asanachitepo zimenezi kuchokera m’masiku a Yoswa mwana wa Nuni,+ mpaka kudzafika tsiku limeneli.

  • Mlaliki 5:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Chinthu chabwino kwambiri ndiponso chokongola chimene ine ndaona, n’chakuti munthu ayenera kudya, kumwa ndi kusangalala, chifukwa cha ntchito yake yonse yovuta+ imene amaigwira mwakhama padziko lapansi pano, kwa masiku onse a moyo wake amene Mulungu woona wam’patsa. Pakuti imeneyo ndiyo mphoto yake.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena