9 Pamenepo Mose analemba chilamulo chimenechi+ ndi kuchipereka kwa ansembe, ana a Levi,+ onyamula likasa la pangano la Yehova.+ Anachiperekanso kwa akulu onse a Isiraeli.
8 Buku la malamulo ili lisachoke pakamwa pako,+ uziliwerenga ndi kusinkhasinkha usana ndi usiku, kuti uonetsetse kuti ukutsatira zonse zolembedwamo.+ Pakuti ukatero, udzakhala ndi moyo wopambana, ndipo udzachita zinthu mwanzeru.+
14 Pamene anali kutulutsa ndalama+ zimene zinali kubwera kunyumba ya Yehova, wansembe Hilikiya+ anapeza buku+ la chilamulo cha Yehova+ loperekedwa ndi dzanja la Mose.+