14 Pamenepo, mizinda imene Afilisitiwo analanda Isiraeli inayamba kubwerera kwa Isiraeli, kuyambira ku Ekironi mpaka ku Gati, ndipo Aisiraeli analanda dera la mizindayo m’manja mwa Afilisiti.
Choncho panakhala mtendere pakati pa Isiraeli ndi Aamori.+