Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yoswa 19:51
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 51 Zimenezi ndiye zigawo za cholowa chimene wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri a mafuko a ana a Isiraeli, anagawira anthu.+ Anagawa dzikolo pochita maere ku Silo+ pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako,+ ndipo anamaliza kuligawa dzikolo.

  • Yoswa 21:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Analankhula nawo ku Silo+ m’dziko la Kanani, kuti: “Kudzera mwa Mose, Yehova analamula kuti tipatsidwe mizinda yoti tizikhalamo, pamodzi ndi malo odyetsera ziweto ozungulira mizindayo, oti tizidyetserako ziweto zathu.”+

  • Yoswa 22:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Zitatero, ana a Rubeni, ana a Gadi, ndi hafu ya fuko la Manase, anachoka ku Silo kumene kunali ana ena a Isiraeli m’dziko la Kanani. Anapita ku Giliyadi,+ dziko lawo limene anapatsidwa ndi Mose molamulidwa ndi Yehova, ndiponso limene anakhazikikamo.+

  • Oweruza 21:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Pamapeto pake anati: “Pajatu ku Silo+ kumachitika chikondwerero cha Yehova chaka ndi chaka. Mzinda wa Silo uli kum’mwera kwa Beteli, chakum’mawa kwa msewu waukulu wochokera ku Beteli kupita ku Sekemu,+ ndiponso chakum’mwera kwa Lebona.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena