34Ndiyeno Mose anachoka m’chipululu cha Mowabu kupita m’phiri la Nebo,+ pamwamba pa Pisiga,+ moyang’anana ndi Yeriko.+ Pamenepo Yehova anayamba kumuonetsa dziko lonse, kuchokera ku Giliyadi mpaka ku Dani.+
20Chotero ana onse a Isiraeli anatuluka,+ kuchokera ku Dani+ mpaka kumunsi ku Beere-seba,+ ndipo khamu lonselo linasonkhana pamodzi mogwirizana+ kwa Yehova ku Mizipa,+ pamodzinso ndi anthu a m’dera la Giliyadi.+
11 Ndiye ine malangizo anga ndi onena kuti: Sonkhanitsa ndithu Isiraeli yense pamaso pako kuyambira ku Dani mpaka ku Beere-seba.+ Akhale ochuluka ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja,+ ndipo iweyo uwatsogolere kunkhondo.+