34Ndiyeno Mose anachoka m’chipululu cha Mowabu kupita m’phiri la Nebo,+ pamwamba pa Pisiga,+ moyang’anana ndi Yeriko.+ Pamenepo Yehova anayamba kumuonetsa dziko lonse, kuchokera ku Giliyadi mpaka ku Dani.+
20Chotero ana onse a Isiraeli anatuluka,+ kuchokera ku Dani+ mpaka kumunsi ku Beere-seba,+ ndipo khamu lonselo linasonkhana pamodzi mogwirizana+ kwa Yehova ku Mizipa,+ pamodzinso ndi anthu a m’dera la Giliyadi.+
29 Kungoti iye sanasiye kutsatira machimo a Yerobowamu+ mwana wa Nebati amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+ Machimo ake anali kulambira ana a ng’ombe agolide.+ Mmodzi wa ana a ng’ombe agolidewo anali ku Beteli, ndipo wina ku Dani.+