-
Yoswa 8:33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
33 Aisiraeli onse, atsogoleri awo,+ akapitawo awo, ndi oweruza awo anasonkhanitsidwa pamodzi. Panalinso alendo okhala pakati pawo.+ Ena anaima mbali iyi ya Likasa, ena anaima mbali inayo, pamaso pa ansembe+ achilevi. Ansembewo anali atanyamula likasa la pangano la Yehova.+ Hafu ya anthuwo inaima m’phiri la Gerizimu,+ ndipo hafu ina inaima m’phiri la Ebala,+ (monga mmene Mose mtumiki wa Yehova analamulira,)+ kuti Aisiraeliwo adalitsidwe+ choyamba.
-