Ekisodo 34:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Ndipo Yehova anadutsa pamaso pa Mose akulengeza kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo+ ndi wachisomo,+ wosakwiya msanga+ ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha+ ndi choonadi.+ Rute 1:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Kenako Naomi anauza apongozi akewo kuti: “Basi bwererani, aliyense apite kunyumba kwa amayi ake. Yehova akusonyezeni kukoma mtima kosatha+ ngati mmenenso inuyo munasonyezera kukoma mtima kumeneko kwa amuna anu amene anamwalira ndiponso kwa ine.+ Salimo 36:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Inu Mulungu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwamtengo wapatali!+Ndipo ana a anthu amabisala mu mthunzi wa mapiko anu.+ Salimo 62:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Komanso kukoma mtima kosatha ndi kwanu, inu Yehova,+Pakuti inu mumabwezera aliyense mogwirizana ndi ntchito zake.+ Maliro 3:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Chifukwa cha kukoma mtima kosatha+ kwa Yehova, ife sitinafafanizidwe,+ ndipo chifundo chake sichidzatha.+
6 Ndipo Yehova anadutsa pamaso pa Mose akulengeza kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo+ ndi wachisomo,+ wosakwiya msanga+ ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha+ ndi choonadi.+
8 Kenako Naomi anauza apongozi akewo kuti: “Basi bwererani, aliyense apite kunyumba kwa amayi ake. Yehova akusonyezeni kukoma mtima kosatha+ ngati mmenenso inuyo munasonyezera kukoma mtima kumeneko kwa amuna anu amene anamwalira ndiponso kwa ine.+
7 Inu Mulungu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwamtengo wapatali!+Ndipo ana a anthu amabisala mu mthunzi wa mapiko anu.+
12 Komanso kukoma mtima kosatha ndi kwanu, inu Yehova,+Pakuti inu mumabwezera aliyense mogwirizana ndi ntchito zake.+
22 Chifukwa cha kukoma mtima kosatha+ kwa Yehova, ife sitinafafanizidwe,+ ndipo chifundo chake sichidzatha.+