2 Samueli 15:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Koma Itai anayankha mfumu kuti: “Pali Yehova, Mulungu wamoyo, komanso pali moyo wanu mbuyanga mfumu,+ kulikonse kumene inu mbuyanga mfumu mudzapita ine mtumiki wanu ndidzapitanso komweko, ndipo ndili wokonzeka ngakhale kufa nanu limodzi!”+ 2 Mafumu 2:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Kenako Eliya anauza Elisa kuti: “Iweyo khala apa, pakuti ine Yehova wandituma ku Beteli.” Koma Elisa anati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo+ ndiponso pali moyo wanu,+ sindikusiyani.”+ Choncho iwo anapita ku Beteli.+ Yeremiya 10:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Koma Yehova ndi Mulungu woonadi.+ Iye ndi Mulungu wamoyo+ ndipo ndi Mfumu mpaka kalekale.+ Dziko lapansi lidzagwedezeka ndi mkwiyo wake,+ ndipo palibe mitundu ya anthu imene idzalimbe pamene iye akuidzudzula.+ Yeremiya 38:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Mfumu Zedekiya inalumbira kwa Yeremiya, ali pamalo obisika kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, amene amatipatsa moyo,+ sindikupha ndipo sindikupereka m’manja mwa anthu awa amene akufuna moyo wako.”+
21 Koma Itai anayankha mfumu kuti: “Pali Yehova, Mulungu wamoyo, komanso pali moyo wanu mbuyanga mfumu,+ kulikonse kumene inu mbuyanga mfumu mudzapita ine mtumiki wanu ndidzapitanso komweko, ndipo ndili wokonzeka ngakhale kufa nanu limodzi!”+
2 Kenako Eliya anauza Elisa kuti: “Iweyo khala apa, pakuti ine Yehova wandituma ku Beteli.” Koma Elisa anati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo+ ndiponso pali moyo wanu,+ sindikusiyani.”+ Choncho iwo anapita ku Beteli.+
10 Koma Yehova ndi Mulungu woonadi.+ Iye ndi Mulungu wamoyo+ ndipo ndi Mfumu mpaka kalekale.+ Dziko lapansi lidzagwedezeka ndi mkwiyo wake,+ ndipo palibe mitundu ya anthu imene idzalimbe pamene iye akuidzudzula.+
16 Mfumu Zedekiya inalumbira kwa Yeremiya, ali pamalo obisika kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, amene amatipatsa moyo,+ sindikupha ndipo sindikupereka m’manja mwa anthu awa amene akufuna moyo wako.”+