22 Koma mwamuna aliyense woipa ndi wopanda pake+ mwa amuna onse amene anatsatira Davide anayamba kunena kuti: “Chifukwa chakuti amenewa sanapite nafe, sitiwapatsa zofunkha zimene talanditsazi. Koma aliyense tingomupatsa mkazi wake ndi ana ake basi, awatenge ndipo azipita.”