28 Chonde, khululukani kulakwa kwa kapolo wanu wamkazi,+ pakuti mosalephera Yehova adzakukhazikitsirani nyumba yachifumu, inu mbuyanga, ndipo idzakhalapo kwa nthawi yaitali,+ chifukwa inu mbuyanga mukumenya nkhondo za Yehova.+ Ndipo mwa inu simudzapezeka choipa chilichonse masiku onse a moyo wanu.+