24 Chotero iwo ananyamuka ndi kupita ku Zifi,+ Sauli atamusiya kumbuyo. Izi zinachitika pamene Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye anali m’chipululu cha Maoni,+ mu Araba,+ kum’mwera kwa Yesimoni.
26Patapita nthawi, amuna a ku Zifi+ anapita kwa Sauli ku Gibeya,+ ndipo anamuuza kuti: “Kodi simukudziwa kuti Davide akubisala kuphiri la Hakila+ moyang’anana ndi Yesimoni?”*+