6 Choncho iye anauza amuna amene anali kuyenda naye kuti: “Sindinayenere m’pang’ono pomwe kuchitira mbuyanga zimenezi pamaso pa Yehova. Iye ndi wodzozedwa+ wa Yehova. Sindinayenere kutambasula dzanja langa ndi kumuukira, pakuti iye ndi wodzozedwa wa Yehova.”+