12 Chotero Davide anapita kukatenga mafupa a Sauli+ ndi mafupa a Yonatani mwana wake kwa anthu a ku Yabesi-giliyadi.+ Anthuwo ndiwo anaba mitembo ya Sauli ndi Yonatani m’bwalo la mzinda wa Beti-sani,+ kumene Afilisiti anali ataipachika,+ tsiku limene anapha Sauli paphiri la Giliboa.+