-
1 Samueli 17:28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Tsopano Eliyabu,+ m’bale wake wamkulu kwambiri wa Davide anamva zimene Davideyo anali kulankhula ndi amunawo. Eliyabu anapsa mtima kwambiri chifukwa cha Davide,+ moti anati: “N’chifukwa chiyani wabwera kuno? Nanga nkhosa zochepa za bambo wasiyira ndani kuchipululu?+ Ine ndikudziwa bwino kudzikuza kwako ndi kuipa kwa mtima wako,+ chifukwa wabwera kuno kuti udzaonerere nkhondo.”+
-