Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 20:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “Mukapita kunkhondo kukamenyana ndi adani anu, musachite nawo mantha mukaona kuti ali ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo,+ ndiponso mukaona kuti adani anuwo ndi ochuluka kwambiri kuposa inu. Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo ali ndi inu.+

  • Yoswa 1:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Monga ndakulamula kale,+ ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usachite mantha kapena kuopa,+ pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.”+

  • 1 Samueli 17:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Koma amuna onse a Isiraeli atangoona mwamunayu anayamba kuthawa, chifukwa anachita naye mantha kwambiri.+

  • Salimo 27:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Yehova ndiye kuwala+ kwanga ndi chipulumutso changa.+

      Ndingaopenso ndani?+

      Yehova ndiye malo a chitetezo cha moyo wanga.+

      Ndingachitenso mantha ndi ndani?+

  • Yesaya 51:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “Ineyo ndi amene ndikukutonthozani anthu inu.+

      “Kodi n’chifukwa chiyani iwe ukuopa munthu woti adzafa,+ ndi mwana wa munthu yemwe adzakhale ngati udzu wobiriwira?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena