28 Zitatero, Samueli anamuuza kuti: “Yehova wang’amba+ ndi kuchotsa ufumu wa Isiraeli kwa iwe lero, ndipo adzaupereka kwa mnzako, munthu woyenerera kuposa iwe.+
13 Choncho Samueli anatenga nyanga ya mafuta+ ndi kum’dzoza pakati pa abale ake. Zitatero, mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa Davide kuyambira tsiku limenelo mpaka m’tsogolo.+ Kenako Samueli ananyamuka kupita ku Rama.+
31 Masiku onse amene mwana wa Jeseyo adzakhala ndi moyo, iweyo ndi ufumu wako sudzakhazikika ayi.+ Choncho tumiza anthu akamugwire ndi kumubweretsa kwa ine, pakuti ayenera kufa ndithu.”+