13 Choncho Samueli anatenga nyanga ya mafuta+ ndi kum’dzoza pakati pa abale ake. Zitatero, mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa Davide kuyambira tsiku limenelo mpaka m’tsogolo.+ Kenako Samueli ananyamuka kupita ku Rama.+
3Nkhondo ya pakati pa nyumba ya Sauli ndi nyumba ya Davide inatenga nthawi yaitali.+ Davide anapitirizabe kukhala wamphamvu+ koma nyumba ya Sauli inali kufookerafookera.+