Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 27:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Yoswayo aziimirira pamaso pa wansembe Eleazara, ndipo Eleazara azifunsira+ chigamulo cha Yehova m’malo mwa Yoswayo pogwiritsa ntchito maere a Urimu.+ Yoswa akalamula, ana onse a Isiraeli ndi khamu lonse azituluka naye, ndipo akalamulanso, onsewo azibwerako limodzi naye.”

  • 1 Samueli 23:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Ndiyeno Davide anayamba kufunsira+ kwa Yehova, kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Afilisitiwa?” Yehova anayankha Davide kuti: “Pita, ukamenyane ndi Afilisitiwo ndipo ukapulumutse Keila.”

  • 2 Samueli 2:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Ndiyeno pambuyo pake, Davide anayamba kufunsira kwa Yehova,+ kuti: “Kodi ndipite ku umodzi mwa mizinda ya Yuda?” Pamenepo Yehova anamuuza kuti: “Pita.” Davide anafunsanso kuti: “Ndipite kuti?” Iye anamuyankha kuti: “Ku Heburoni.”+

  • 1 Mbiri 14:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndiyeno Davide anafunsira kwa Mulungu+ kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Afilisitiwa? Kodi muwaperekadi m’manja mwanga?” Pamenepo Yehova anauza Davide kuti: “Pita, amenewa ndiwaperekadi m’manja mwako.”

  • Miyambo 3:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Uzim’kumbukira m’njira zako zonse,+ ndipo iye adzawongola njira zako.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena