22 Atapita ku Negebu,+ anakafika ku Heburoni.+ Kumeneko anapezako Ahimani, Sesai ndi Talimai,+ mbadwa za Anaki.*+ Mzinda wa Heburoni+ unamangidwa zaka 7 mzinda wa Zowani+ wa ku Iguputo usanamangidwe.
14 N’chifukwa chake mzinda wa Heburoni uli cholowa cha Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi, kufikira lero. Anam’patsa mzindawo chifukwa iye anatsatira Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mtima wake wonse.+
7 Choncho anasankha mizinda ina kuti ikhale yopatulika. Mizinda yake inali Kedesi+ ku Galileya m’dera lamapiri la Nafitali, Sekemu+ m’dera lamapiri la Efuraimu, Kiriyati-ariba,+ kutanthauza Heburoni, m’dera lamapiri la Yuda.