-
Deuteronomo 9:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Sikuti mukulowa m’dziko ili kukalitenga kukhala lanu chifukwa cha kulungama kwanu+ kapena chifukwa cha kuwongoka mtima kwanu.+ Yehova Mulungu wanu akukankhira mitundu iyi kutali ndi inu, kwenikweni chifukwa cha kuipa kwawo,+ ndiponso kuti Yehova akwaniritse mawu onse amene analumbirira makolo anu Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo.+
-
-
Yoswa 23:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 “Tsopano taonani! Ine ndatsala pang’ono kufa.+ Inu mukudziwa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwaniritsidwe. Onse akwaniritsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mawu amodzi omwe sanakwaniritsidwe.+
-