Genesis 25:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Yehova anamuyankha kuti: “M’mimba mwako+ muli mitundu iwiri ya anthu, ndipo mitundu iwiri imene idzatuluka m’mimba mwakoyo idzakhala yosiyana.+ Mtundu wina udzakhala wamphamvu kuposa mtundu winawo,+ ndipo wamkulu adzatumikira wamng’ono.”+ Genesis 27:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Mafuko akutumikire ndipo mitundu ya anthu ikugwadire.+ Ukhale mbuye wa abale ako, ndipo ana a mayi ako akugwadire.+ Aliyense wokutemberera atembereredwe, ndipo aliyense wokudalitsa adalitsidwe.”+ Genesis 27:37 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 37 Koma Isaki anayankha Esau kuti: “Taona, iye uja ndamuika kukhala mbuye wako.+ Ndamupatsanso abale ake onse kuti akhale atumiki ake.+ Komanso ndam’dalitsira zokolola zake ndi vinyo wake watsopano.+ Nanga chatsalanso n’chiyani choti ndikuchitire mwana wanga?” Numeri 24:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Edomu adzalandidwa,+Ndithu Seiri+ adzalandidwa ndi adani ake,+Pamene Isiraeli akuonetsa kulimba mtima kwake.
23 Yehova anamuyankha kuti: “M’mimba mwako+ muli mitundu iwiri ya anthu, ndipo mitundu iwiri imene idzatuluka m’mimba mwakoyo idzakhala yosiyana.+ Mtundu wina udzakhala wamphamvu kuposa mtundu winawo,+ ndipo wamkulu adzatumikira wamng’ono.”+
29 Mafuko akutumikire ndipo mitundu ya anthu ikugwadire.+ Ukhale mbuye wa abale ako, ndipo ana a mayi ako akugwadire.+ Aliyense wokutemberera atembereredwe, ndipo aliyense wokudalitsa adalitsidwe.”+
37 Koma Isaki anayankha Esau kuti: “Taona, iye uja ndamuika kukhala mbuye wako.+ Ndamupatsanso abale ake onse kuti akhale atumiki ake.+ Komanso ndam’dalitsira zokolola zake ndi vinyo wake watsopano.+ Nanga chatsalanso n’chiyani choti ndikuchitire mwana wanga?”
18 Edomu adzalandidwa,+Ndithu Seiri+ adzalandidwa ndi adani ake,+Pamene Isiraeli akuonetsa kulimba mtima kwake.