16 Koma mwamuna wake anali kumutsatira. Iye anali kumutsatira pambuyo akulira mpaka kukafika ku Bahurimu.+ Kenako Abineri anamuuza kuti: “Bwerera!” Pamenepo iye anabwerera.
5 Ndiyeno Mfumu Davide inafika ku Bahurimu.+ Kumeneko inaona mwamuna wina wa m’banja la Sauli, dzina lake Simeyi,+ mwana wa Gera akutuluka ndipo anali kulankhula mawu onyoza.+
16 Kenako Simeyi+ mwana wa Gera,+ wa fuko la Benjamini, wochokera ku Bahurimu,+ pamodzi ndi amuna a ku Yuda anapita mofulumira kukakumana ndi Mfumu Davide.