29 Mlandu umenewu ubwerere pamutu+ pa Yowabu ndi pa nyumba yonse ya bambo ake. M’nyumba ya Yowabu+ simudzasowa munthu wa nthenda yakukha kumaliseche+ ndiponso wakhate.+ Simudzasowanso mwamuna wogwira ndodo yowombera nsalu,+ wokanthidwa ndi lupanga kapena wosowa mkate!”+