Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:43
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 43 Kondwerani, mitundu inu, pamodzi ndi anthu ake,+

      Pakuti adzabwezera magazi a atumiki ake,+

      Ndipo adzabwezera chilango kwa adani ake,+

      Nadzaphimba machimo a dziko la anthu ake.”

  • Oweruza 9:57
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 57 Ndipo zoipa zonse za amuna a m’Sekemu, Mulungu anachititsa kuti ziwabwerere pamutu pawo, kuti temberero+ la Yotamu+ mwana wa Yerubaala,+ liwagwere.+

  • 2 Samueli 1:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Kenako Davide anamuuza kuti: “Mlandu wa magazi ako ukhale pamutu pako,+ chifukwa wadzichitira wekha umboni+ ponena kuti, ‘Ineyo ndapha wodzozedwa wa Yehova.’”+

  • 1 Mafumu 2:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Zikadzachitika kuti tsiku lina wachoka n’kudutsa chigwa* cha Kidironi,+ udziwiretu kuti udzafa ndithu.+ Mlandu wa magazi ako udzakhala pamutu pako.”+

  • Salimo 7:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Mavuto ake adzabwerera pamutu pake,+

      Ndipo chiwawa chake chidzatsikira paliwombo pake.+

  • Salimo 55:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Koma inu Mulungu, mudzatsitsira oipa kumanda.+

      Ndipo anthu amene ali ndi mlandu wa magazi komanso anthu achinyengo, sadzakwanitsa kukhala ngakhale hafu ya moyo wawo.+

      Koma ine ndidzakhulupirira inu.+

  • Salimo 94:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Iye adzawabwezera zoipa zawo,+

      Ndipo adzawakhalitsa chete mwa kuwadzetsera masoka okonza okha.+

      Yehova Mulungu wathu adzawakhalitsa chete.+

  • Miyambo 5:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Woipa adzagwidwa ndi zolakwa zake zomwe,+ ndipo adzamangidwa m’zingwe za tchimo lake lomwe.+

  • Miyambo 28:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Munthu wolemedwa ndi mlandu wokhetsa magazi a munthu adzakhala wothawathawa mpaka kumanda.+ Anthu asamugwire n’cholinga choti amuletse.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena