Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yoswa 2:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Aliyense amene adzatuluke pakhomo la nyumba yako kupita panja,+ magazi ake adzakhala pamutu pake. Ife tidzakhala opanda mlandu. Koma ngati aliyense amene adzakhalebe limodzi nawe m’nyumbamu adzaphedwe, magazi ake adzakhale pamutu pathu.

  • Oweruza 9:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Mulungu analola zimenezi kuti chiwawa chimene anachitira ana aamuna 70 a Yerubaala chiwabwerere pamutu pawo,+ ndi kuti aike magazi a anawo pa Abimeleki m’bale wawo chifukwa ndiye anawapha.+ Analolanso zimenezi kuti chiwawacho chibwerere pamutu pa nzika za Sekemu, chifukwa zinalimbikitsa+ Abimeleki kuti aphe abale ake.

  • 2 Samueli 4:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndiye kuli bwanji pamene anthu oipa+ apha munthu wolungama pabedi m’nyumba yake? Kodi sindiyenera kufuna magazi ake m’manja mwanu+ ndi kukuchotsani padziko?”+

  • 1 Mafumu 2:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Zikadzachitika kuti tsiku lina wachoka n’kudutsa chigwa* cha Kidironi,+ udziwiretu kuti udzafa ndithu.+ Mlandu wa magazi ako udzakhala pamutu pako.”+

  • Ezekieli 18:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Iye amakongoza zinthu zake mwa katapira+ ndipo amalandira chiwongoladzanja.+ Ndithudi iye sadzakhala ndi moyo chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi.+ Adzaphedwa ndithu, ndipo magazi ake adzakhala pamutu pake.+

  • Machitidwe 18:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Koma iwo atapitiriza kumutsutsa ndi kulankhula monyoza,+ iye anakutumula zovala zake+ ndi kuwauza kuti: “Magazi anu+ akhale pamitu panu. Ine ndilibe mlandu.+ Kuyambira tsopano ndizipita kwa anthu a mitundu ina.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena