-
2 Mafumu 10:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Pamenepo Yehu anawalemberanso kalata yachiwiri kuti: “Ngati muli kumbali yanga+ ndipo ngati muzimvera mawu anga, dulani mitu ya ana aamuna+ a mbuye wanu, ndipo mawa nthawi ngati yomwe ino mubwere nayo kwa ine ku Yezereeli.”+
Ana aamuna a mfumuwo, omwe analipo 70, anali ndi akuluakulu a mumzindawo omwe anali kuwasamalira.
-
-
2 Mafumu 10:25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Yehu atangomaliza kupereka nsembe yopserezayo, nthawi yomweyo anauza asilikali ake othamanga ndi othandiza pamagaleta kuti: “Lowani, apheni! Pasapezeke ndi mmodzi yemwe wotuluka panja.”+ Atamva zimenezi, asilikali ake othamanga ndi othandiza pamagaleta+ aja anayamba kupha anthuwo ndi lupanga n’kumaponyera mitembo yawo panja. Anakafika mpaka m’chipinda chamkati mwa kachisiyo chotchedwa mzinda wa Baala.
-