Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Yehova adzakuyendetsa+ pamodzi ndi mfumu+ yako imene udzadziikira, kukupititsa ku mtundu umene iweyo kapena makolo ako simunaudziwe. Kumeneko udzatumikira milungu ina, yamtengo kapena yamwala.+

  • 2 Mafumu 17:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 M’chaka cha 9 cha Hoshiya, mfumu ya Asuri inalanda Samariya+ n’kutenga Aisiraeli kupita nawo ku Asuri.+ Mfumuyo inakaika Aisiraeliwo ku Hala+ ndi ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani,+ ndiponso m’mizinda ya Amedi.+

  • 2 Mafumu 25:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Mfumu ya Babuloyo inapha anthuwo+ ku Ribila m’dziko la Hamati.+ Choncho Ayuda anachoka kudziko lawo n’kupita ku ukapolo.+

  • Danieli 9:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Inu Yehova ndinu wolungama, koma ife manyazi aphimba nkhope zathu lero.+ Manyazi aphimba nkhope za amuna a mu Yuda, anthu a ku Yerusalemu ndi anthu onse a ku Isiraeli, amene ali pafupi ndiponso amene ali kumayiko onse akutali kumene munawabalalitsira chifukwa cha zinthu zosakhulupirika zimene anakuchitirani.+

  • Luka 21:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Anthu adzaphedwa ndi lupanga ndiponso kutengedwa ukapolo kupita nawo ku mitundu ina yonse.+ Anthu a mitundu ina adzapondaponda Yerusalemu, kufikira nthawi zoikidwiratu+ za anthu a mitundu inawo zitakwanira.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena