Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:64
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 64 “Yehova adzakumwazani mwa anthu a mitundu yonse kuchokera kumalekezero ena a dziko mpaka kumalekezero enanso a dziko.+ Kumeneko mukatumikira milungu ina imene inuyo kapena makolo anu simunaidziwe, milungu yamtengo ndi milungu yamwala.+

  • Salimo 79:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 79 Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowa m’dziko limene ndilo cholowa chanu.+

      Aipitsa kachisi wanu woyera.+

      Awononga Yerusalemu ndi kumusandutsa bwinja.+

  • Yesaya 63:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Kwa kanthawi kochepa, anthu anu oyera+ anali ndi zinthu. Koma adani athu apondaponda malo anu opatulika.+

  • Danieli 9:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 “Mesiyayo* adzasungira anthu ambiri pangano+ kwa mlungu umodzi,+ kenako pakatikati pa mlunguwo adzathetsa nsembe zanyama ndi nsembe zina zoperekedwa ngati mphatso.+

      “Wowonongayo+ adzabwera pamapiko a zinthu zonyansa, ndipo zimene Mulungu wagamula zidzakhuthulidwanso pa chowonongedwacho+ kufikira chitafafanizidwa.”

  • Zekariya 12:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pa tsiku limenelo,+ Yerusalemu ndidzamusandutsa mwala wotopetsa+ kwa anthu a mitundu yonse. Onse onyamula mwala umenewo, ndithu adzatemekatemeka koopsa. Anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi adzasonkhana pamodzi kuti amuukire.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena