2 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Munthu aliyense mwa ana a Isiraeli, ndiponso mlendo aliyense wokhala mu Isiraeli, wopereka mwana wake aliyense kwa Moleki,*+ aziphedwa ndithu. Nzika za m’dziko lanu zizimupha mwa kum’ponya miyala.
5 Ndidzafafaniza anthu amene akugwadira khamu la zinthu zakuthambo pamadenga* a nyumba zawo,+ ndiponso amene akugwada ndi kulumbira+ kuti adzakhala okhulupirika kwa Yehova+ koma amakhalanso akulumbira m’dzina la Malikamu.+