-
Yeremiya 8:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Mafupawo adzawamwaza poyera ndipo dzuwa, mwezi, ndi makamu onse akumwamba zidzawala pa iwo. Zinthu zimenezi ndi zimene iwo anali kuzikonda, kuzitumikira, kuzitsatira,+ kuzipembedza, ndi kuziweramira.+ Mafupawo sadzasonkhanitsidwa pamodzi kapena kuikidwa m’manda. Iwo adzakhala ngati manyowa panthaka.”+
-
-
Ezekieli 8:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Chotero anandipititsa kubwalo lamkati la nyumba ya Yehova.+ Ndiyeno ndinaona kuti pakhomo lolowera m’kachisi wa Yehova, pakati pa khonde ndi guwa lansembe,+ panali amuna pafupifupi 25+ atafulatira kachisi wa Yehova.+ Nkhope zawo anali atazilozetsa kum’mawa ndipo anali kugwadira dzuwa atayang’ana kum’mawa.+
-