Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 9:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Ndipo mtembo wa Yezebeli, ndithu udzasanduka manyowa+ m’munda wa ku Yezereeli kuti anthu asadzanene kuti: “Uyu ndi Yezebeli.”’”+

  • Salimo 83:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Iwo anawonongedwa ku Eni-dori.+

      Anasanduka manyowa a m’nthaka.+

  • Yeremiya 9:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 “Unene kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Mitembo ya anthu idzangoti mbwee panthaka ngati manyowa. Idzakhala ngati tirigu amene angomumweta kumene koma palibe munthu womusonkhanitsa pamodzi.”’”+

  • Yeremiya 16:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 ‘Iwo adzafa ndi matenda oopsa+ ndipo sadzawalira maliro+ kapena kuikidwa m’manda+ koma adzakhala ngati manyowa panthaka.+ Iwo adzafa ndi lupanga ndiponso njala yaikulu.+ Mitembo yawo idzakhala chakudya cha zolengedwa zouluka zam’mlengalenga ndi zilombo zakutchire.’+

  • Yeremiya 25:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Pa tsiku limenelo padzakhala anthu ophedwa ndi Yehova kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kufikanso kumalekezero ena a dziko lapansi.+ Sadzawalira maliro, kuwasonkhanitsa pamodzi, kapena kuwaika m’manda.+ Iwo adzakhala ngati manyowa panthaka.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena