Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 4:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Musamale kuti musakweze maso anu kuthambo ndi kuona dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la zinthu zakuthambo, zimene Yehova Mulungu wanu wazipereka kwa anthu onse okhala pansi pa thambo lonse,+ n’kunyengeka nazo, kuzigwadira ndi kuyamba kuzitumikira.+

  • Deuteronomo 17:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 moti akupita kukalambira milungu ina ndi kuigwadira, kapena kugwadira dzuwa, mwezi kapena khamu lonse la zinthu zakuthambo,+ chinthu chimene ine sindinakulamuleni,+

  • 2 Mafumu 17:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Anasiya malamulo onse+ a Yehova Mulungu wawo n’kudzipangira zifaniziro ziwiri za ana a ng’ombe,+ zopangidwa ndi zitsulo zosungunula,+ komanso mzati wopatulika.+ Anayamba kugwadira khamu lonse la zinthu zakuthambo+ ndi kutumikira Baala.+

  • 2 Mafumu 21:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Choncho iye anamanganso malo okwezeka amene Hezekiya bambo ake anachotsa.+ Anamanga maguwa ansembe a Baala n’kumanga mzati wopatulika, monga momwe Ahabu+ mfumu ya Isiraeli anachitira. Iye anayambanso kugwadira+ khamu lonse la zinthu zakuthambo,+ n’kumazitumikira.+

  • Yeremiya 7:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Kodi mungamabe,+ kupha,+ kuchita chigololo,+ kulumbira monama,+ kufukiza nsembe zautsi kwa Baala+ ndi kutsatira milungu ina imene simunali kuidziwa,+

  • Yeremiya 19:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 ‘Nyumba za mu Yerusalemu ndi nyumba za mafumu a Yuda zidzakhala zodetsedwa ngati Tofeti.+ Zimenezi ndi nyumba zonse zimene pamadenga ake anali kufukizirapo nsembe zautsi kwa makamu akumwamba+ ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa milungu ina.’”+

  • Zefaniya 1:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ndidzafafaniza anthu amene akugwadira khamu la zinthu zakuthambo pamadenga* a nyumba zawo,+ ndiponso amene akugwada ndi kulumbira+ kuti adzakhala okhulupirika kwa Yehova+ koma amakhalanso akulumbira m’dzina la Malikamu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena