Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 17:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 moti akupita kukalambira milungu ina ndi kuigwadira, kapena kugwadira dzuwa, mwezi kapena khamu lonse la zinthu zakuthambo,+ chinthu chimene ine sindinakulamuleni,+

  • 2 Mafumu 17:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Anasiya malamulo onse+ a Yehova Mulungu wawo n’kudzipangira zifaniziro ziwiri za ana a ng’ombe,+ zopangidwa ndi zitsulo zosungunula,+ komanso mzati wopatulika.+ Anayamba kugwadira khamu lonse la zinthu zakuthambo+ ndi kutumikira Baala.+

  • Yeremiya 8:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Mafupawo adzawamwaza poyera ndipo dzuwa, mwezi, ndi makamu onse akumwamba zidzawala pa iwo. Zinthu zimenezi ndi zimene iwo anali kuzikonda, kuzitumikira, kuzitsatira,+ kuzipembedza, ndi kuziweramira.+ Mafupawo sadzasonkhanitsidwa pamodzi kapena kuikidwa m’manda. Iwo adzakhala ngati manyowa panthaka.”+

  • Ezekieli 8:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Chotero anandipititsa kubwalo lamkati la nyumba ya Yehova.+ Ndiyeno ndinaona kuti pakhomo lolowera m’kachisi wa Yehova, pakati pa khonde ndi guwa lansembe,+ panali amuna pafupifupi 25+ atafulatira kachisi wa Yehova.+ Nkhope zawo anali atazilozetsa kum’mawa ndipo anali kugwadira dzuwa atayang’ana kum’mawa.+

  • Zefaniya 1:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ndidzafafaniza anthu amene akugwadira khamu la zinthu zakuthambo pamadenga* a nyumba zawo,+ ndiponso amene akugwada ndi kulumbira+ kuti adzakhala okhulupirika kwa Yehova+ koma amakhalanso akulumbira m’dzina la Malikamu.+

  • Machitidwe 7:43
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 43 Inutu munali kunyamula chihema cha Moloki+ ndi nyenyezi+ ya mulungu Refani, mafano amene munapanga kuti muziwalambira. Chotero ndidzakupitikitsirani+ kutali kupitirira Babulo.’

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena