-
2 Mafumu 23:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Mfumuyo inachotsa ntchito ansembe a milungu yachilendo, amene mafumu a Yuda anawaika kuti azifukiza nsembe yautsi pamalo okwezeka m’mizinda ya Yuda ndi malo ozungulira Yerusalemu. Inachotsanso ntchito ansembe ofukiza nsembe yautsi kwa Baala,+ kwa dzuwa, kwa mwezi, kwa magulu a nyenyezi, ndi kwa khamu lonse la zinthu zakuthambo.+
-
-
Ezekieli 8:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Chotero anandipititsa kubwalo lamkati la nyumba ya Yehova.+ Ndiyeno ndinaona kuti pakhomo lolowera m’kachisi wa Yehova, pakati pa khonde ndi guwa lansembe,+ panali amuna pafupifupi 25+ atafulatira kachisi wa Yehova.+ Nkhope zawo anali atazilozetsa kum’mawa ndipo anali kugwadira dzuwa atayang’ana kum’mawa.+
-